8 Mukapereka nsembe nyama yakhungu, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.” Mukapereka nsembe nyama yolumala kapena yodwala, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.”’”+
“Pitani nayo kwa bwanamkubwa wanu. Kodi akakondwera nanu? Kapena kodi akakulandirani bwino?” watero Yehova wa makamu.