Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 19:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Muzikhala ndi masikelo olondola,+ miyala yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu, muyezo wolondola wa efa ndi muyezo wolondola wa hini.* Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo.

  • Deuteronomo 25:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Muyezo wako woyezera kulemera kwa chinthu uzikhala wolondola ndi woyenera. Muyezo wako wa efa uzikhala wolondola ndi woyenera kuti masiku ako achuluke m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+

  • Miyambo 20:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndiponso miyezo iwiri yosiyana ya efa,*+ zonsezi n’zonyansa kwa Yehova.+

  • Ezekieli 45:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 ‘Anthu inu muzikhala ndi masikelo olondola, muyezo wa efa* wolondola ndi mitsuko* yoyezera yolondola.+

  • Amosi 8:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Inu mukunena kuti: ‘Kodi mwezi watsopano utha liti+ kuti tiyambe kugulitsa chakudya?*+ Komanso sabata+ litha liti kuti tiyambe kuchepetsa muyezo wogulitsira zinthu,+ kukweza mtengo ndi kubera wogula mwa kugwiritsa ntchito masikelo achinyengo?+

  • Mika 6:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kodi m’nyumba ya munthu woipa mukupezekabe chuma chopezedwa mopanda chilungamo,+ ndiponso muyezo woperewera wa efa* umene ndi wosaloleka?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena