8 Chifukwa chakuti iwe unafunkha mitundu yambiri ya anthu, anthu onse otsala a m’mitunduyo adzafunkha zinthu zako.+ Iwo adzateronso chifukwa unakhetsa magazi a mtundu wa anthu komanso unachitira chiwawa dziko lapansi, tauni ndi anthu onse okhala mmenemo.+