Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 32:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pakuti nsanja yokhalamo yasiyidwa,+ piringupiringu amene anali mumzindamo watha. Ofeli+ ndi nsanja ya mlonda zasanduka tchire. Mpaka kalekale zidzakhala malo osangalalako mbidzi, ndi odyetserako ziweto,

  • Yeremiya 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, malo opanda wokhalamo.+

  • Maliro 1:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Njira zopita ku Ziyoni zikulira, chifukwa palibe amene akupita kuchikondwerero.+

      Zipata zake zonse zasiyidwa.+ Ansembe+ ake akuusa moyo.*

      Anamwali ake agwidwa ndi chisoni,+ ndipo iyeyo akumva kuwawa mumtima.

  • Maliro 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Zipata+ zake zamira munthaka. Wawononga mipiringidzo yake ndipo waithyolathyola.

      Mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa mitundu ina.+ Malamulo sakutsatiridwa.+

      Aneneri ake sakuonanso masomphenya ochokera kwa Yehova.+

  • Mika 1:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Zilonda zake n’zosachiritsika+ ndipo zafalikira mpaka kukafika ku Yuda.+ Mliri umenewu wakafika pachipata cha anthu amtundu wanga ku Yerusalemu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena