2 Ndikanakonda kukhala ndi malo a m’chipululu ogona anthu apaulendo.+ Pamenepo ndikanasiya anthu anga ndi kuwachokera, pakuti onsewo ndi achigololo,+ gulu la anthu ochita zachinyengo.+
13 “Anthu inu mwalima zoipa+ ndipo mwakolola kusalungama.+ Mwadya zipatso za zochita zanu zachinyengo,+ pakuti munali kudalira njira zanu+ ndi kuchuluka kwa anthu anu amphamvu.+