11 Anthu onse a mu Isiraeli aphwanya malamulo anu ndipo apatuka mwa kusamvera mawu anu.+ Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro+ amene analembedwa m’chilamulo cha Mose, mtumiki wa Mulungu woona, pakuti takuchimwirani.
51 “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+