10 Pamenepo Yehova anasokoneza adaniwo pamaso pa Aisiraeli.+ Ndiyeno Aisiraeli anayamba kupha adaniwo kwadzaoneni ku Gibeoni,+ ndi kuwathamangitsa kulowera kuchitunda cha Beti-horoni. Ndipo anapitiriza kuwapha mpaka kukafika ku Azeka+ ndi ku Makeda.+