9 ‘Likatigwera tsoka,+ lupanga, chiweruzo chowawa, mliri+ kapena njala,+ tiziima pamaso pa nyumba iyi+ ndi pamaso panu (popeza dzina lanu+ lili m’nyumba iyi), kuti tifuulire inu kuti mutithandize m’masautso athu, ndipo inu muzimva ndi kutipulumutsa.’+