23 Ndiyeno anayamba kulankhula kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Atumiki anu+ amene akuyenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse,+ inu mumawasungira pangano ndi kukoma mtima kosatha.+