Genesis 33:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Koma Yakobo anati: “Monga mukudziwa mbuyanga, anawa ndi osakhwima, komanso ndili ndi nkhosa ndi ng’ombe zoyamwitsa.+ Tikaziyendetsa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, ndithu zifa zonse.+ Yohane 10:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ine ndine m’busa wabwino, nkhosa zanga ndimazidziwa,+ izonso zimandidziwa,+ Yohane 10:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Ndili ndi nkhosa zina+ zimene sizili za khola ili,+ zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga,+ ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.+ 1 Petulo 5:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Wetani+ gulu la nkhosa za Mulungu+ lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.+ Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake,+ koma ndi mtima wonse.
13 Koma Yakobo anati: “Monga mukudziwa mbuyanga, anawa ndi osakhwima, komanso ndili ndi nkhosa ndi ng’ombe zoyamwitsa.+ Tikaziyendetsa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, ndithu zifa zonse.+
16 “Ndili ndi nkhosa zina+ zimene sizili za khola ili,+ zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga,+ ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.+
2 Wetani+ gulu la nkhosa za Mulungu+ lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.+ Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake,+ koma ndi mtima wonse.