7 Kodi Yehova adzakondwera ndi masauzande a nkhosa zamphongo? Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande makumimakumi?+ Kapena kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa chifukwa cha cholakwa changa?+ Kodi ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa?