-
Nehemiya 13:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Masiku amenewo ku Yuda ndinaona anthu akuponda moponderamo mphesa tsiku la sabata.+ Anali kubweretsa mbewu ndi kuzikweza+ pa abulu.+ Analinso kukweza pa abuluwo vinyo, mphesa, nkhuyu+ ndi katundu wosiyanasiyana ndipo anali kubwera nazo ku Yerusalemu tsiku la sabata.+ Ine ndinawadzudzula pa tsiku limene anali kugulitsa zinthu zimenezi.
-
-
Yesaya 58:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 “Mukabweza phazi lanu chifukwa cha sabata, kuti musiye kuchita zokonda zanu pa tsiku langa lopatulika,+ sabatalo mukalitcha tsiku losangalatsa kwambiri, tsiku lopatulika ndi lolemekezeka la Yehova,+ ndipo mukalilemekeza m’malo moyenda njira zanu, m’malo mopeza zinthu zosangalatsa inuyo, ndiponso m’malo molankhula zopanda pake,
-