7 Ine ndine Yehova wa makamu ndipo Isiraeli ndi munda wanga wa mpesa.+ Amuna a ku Yuda ndiwo mitengo ya mpesa imene ndinali kuikonda.+ Ine ndinali kuyembekezera chilungamo+ koma ndinaona anthu akuphwanya malamulo. Ndinali kuyembekezera zolungama koma ndinaona anthu akulira.”+
14 Zimene zinagwera paminga, ndi anthu amene amva mawu a Mulungu. Koma chifukwa chotengeka ndi nkhawa, chuma ndi zosangalatsa za moyo uno,+ amalephera kukula bwino, ndipo zipatso zawo sizikhwima.+