1 Samueli 19:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Sauli nayenso anavula zovala zake, ndipo nayenso anayamba kuchita zinthu ngati mneneri pamaso pa Samueli. Iye anagwa pansi ndi kugona pomwepo ali wosavala* usana wonse ndi usiku wonse.+ N’chifukwa chake pali mawu okuluwika akuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+ Mika 1:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Chifukwa cha zimenezi ndidzalira ndi kufuula.+ Ndidzayenda wopanda nsapato komanso wosavala.+ Ndidzalira ngati mimbulu ndi kumva chisoni ngati nthiwatiwa zazikazi. Aheberi 11:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Anaponyedwa miyala,+ anayesedwa,+ anachekedwa pakati ndi macheka, anaphedwa+ mwankhanza ndi lupanga, anayendayenda atavala zikopa za nkhosa+ ndi zikopa za mbuzi pamene anali osowa,+ pamene anali m’masautso+ komanso pamene anali kuzunzidwa.+
24 Sauli nayenso anavula zovala zake, ndipo nayenso anayamba kuchita zinthu ngati mneneri pamaso pa Samueli. Iye anagwa pansi ndi kugona pomwepo ali wosavala* usana wonse ndi usiku wonse.+ N’chifukwa chake pali mawu okuluwika akuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+
8 Chifukwa cha zimenezi ndidzalira ndi kufuula.+ Ndidzayenda wopanda nsapato komanso wosavala.+ Ndidzalira ngati mimbulu ndi kumva chisoni ngati nthiwatiwa zazikazi.
37 Anaponyedwa miyala,+ anayesedwa,+ anachekedwa pakati ndi macheka, anaphedwa+ mwankhanza ndi lupanga, anayendayenda atavala zikopa za nkhosa+ ndi zikopa za mbuzi pamene anali osowa,+ pamene anali m’masautso+ komanso pamene anali kuzunzidwa.+