19 Ndiyeno mdima utafika pazipata za Yerusalemu, sabata lisanayambe, ndinapereka lamulo ndipo zitseko zinayamba kutsekedwa.+ Ndinalamulanso kuti asatsegule zitsekozo kufikira sabata litatha. Ndipo ndinaika ena mwa atumiki anga m’zipata kuti munthu asalowe ndi katundu tsiku la sabata.+