Deuteronomo 28:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Yehova adzakulanga ndi chifuwa chachikulu,+ kuphwanya kwa thupi koopsa, kutupa, kutentha thupi kwambiri, lupanga,+ mphepo yotentha yowononga mbewu+ ndi matenda a mbewu.+ Zimenezi zidzakusautsa kufikira utawonongeka. Yeremiya 32:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Taonani! Anthu abwera kumzinda uno ndipo amanga ziunda zomenyerapo nkhondo+ kuti aulande,+ moti uperekedwa m’manja mwa Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu.+ Anthu adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri.+ Zimene munanena zachitika ndipo ndi izi mukuzionazi.+ Ezekieli 7:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Lupanga+ lili panja ndipo mliri ndi njala zili mkati.+ Yemwe ali kutchire adzaphedwa ndi lupanga, ndipo amene ali mumzinda njala ndi mliri zidzawasakaza.+
22 Yehova adzakulanga ndi chifuwa chachikulu,+ kuphwanya kwa thupi koopsa, kutupa, kutentha thupi kwambiri, lupanga,+ mphepo yotentha yowononga mbewu+ ndi matenda a mbewu.+ Zimenezi zidzakusautsa kufikira utawonongeka.
24 Taonani! Anthu abwera kumzinda uno ndipo amanga ziunda zomenyerapo nkhondo+ kuti aulande,+ moti uperekedwa m’manja mwa Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu.+ Anthu adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri.+ Zimene munanena zachitika ndipo ndi izi mukuzionazi.+
15 Lupanga+ lili panja ndipo mliri ndi njala zili mkati.+ Yemwe ali kutchire adzaphedwa ndi lupanga, ndipo amene ali mumzinda njala ndi mliri zidzawasakaza.+