2 Mbiri 36:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwatumizira machenjezo kudzera mwa amithenga ake.+ Anawatumiza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo+ ndiponso malo ake okhala.+ Salimo 81:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Haa! Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda m’njira zanga.+ Yeremiya 7:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Tsopano chifukwa chakuti mwapitiriza kuchita ntchito zimenezi,’ watero Yehova, ‘ndipo ndinali kukulankhulani nthawi zonse, kudzuka m’mamawa ndi kukulankhulani,+ koma inu osamva,+ kukuitanani koma inu osandiyankha,+ Yeremiya 11:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Inetu ndinalangiza makolo anu pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo+ ndipo ndikupitiriza kutero. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwalangiza kuti: “Muzimvera mawu anga.”+ Yeremiya 13:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Anthu oipa amenewa akukana kumvera mawu anga.+ Iwo akupitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndipo akutsatira milungu ina kuti aitumikire ndi kuigwadira.+ Anthu amenewa adzakhala ngati lamba ameneyu amene sangagwirenso ntchito iliyonse.’ Yeremiya 16:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Ndipo inu mwachita zinthu zoipa kwambiri kuposa makolo anu.+ Aliyense wa inu akupitiriza kuumitsa mtima+ wake woipawo ndipo simukundimvera.+
15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwatumizira machenjezo kudzera mwa amithenga ake.+ Anawatumiza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo+ ndiponso malo ake okhala.+
13 Haa! Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda m’njira zanga.+
13 Tsopano chifukwa chakuti mwapitiriza kuchita ntchito zimenezi,’ watero Yehova, ‘ndipo ndinali kukulankhulani nthawi zonse, kudzuka m’mamawa ndi kukulankhulani,+ koma inu osamva,+ kukuitanani koma inu osandiyankha,+
7 Inetu ndinalangiza makolo anu pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo+ ndipo ndikupitiriza kutero. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwalangiza kuti: “Muzimvera mawu anga.”+
10 Anthu oipa amenewa akukana kumvera mawu anga.+ Iwo akupitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndipo akutsatira milungu ina kuti aitumikire ndi kuigwadira.+ Anthu amenewa adzakhala ngati lamba ameneyu amene sangagwirenso ntchito iliyonse.’
12 Ndipo inu mwachita zinthu zoipa kwambiri kuposa makolo anu.+ Aliyense wa inu akupitiriza kuumitsa mtima+ wake woipawo ndipo simukundimvera.+