10 Pakuti mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri udzatsala wokhawokha. Malo odyetserako ziweto adzakhala opanda kanthu ndipo adzasiyidwa ngati chipululu.+ Kumeneko mwana wa ng’ombe azidzadya msipu ndipo azidzagona pansi. Iye adzadya nthambi zake.+