40 Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya, pamene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anamumasula ku Rama.+ Yeremiya anali womangidwa maunyolo a m’manja pamene Nebuzaradani anamutenga pakati pa anthu a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene anali kupita ku ukapolo ku Babulo.+