Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 36:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwatumizira machenjezo kudzera mwa amithenga ake.+ Anawatumiza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo+ ndiponso malo ake okhala.+

  • Yesaya 65:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,*+ amene akuyenda m’njira yoipa+ potsatira maganizo awo,+

  • Yeremiya 7:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 kuchokera tsiku limene makolo anu anatuluka m’dziko la Iguputo kufikira lero.+ Ndinapitiriza kukutumizirani atumiki anga onse aneneri, tsiku ndi tsiku ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza.+

  • Yeremiya 25:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Yehova anakutumizirani atumiki ake onse aneneri. Anali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza, koma inu simunawamvere+ kapena kutchera khutu lanu kuti mumvetsere.+

  • Yeremiya 26:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 komanso kumvera mawu a atumiki anga aneneri amene ndikuwatumiza kwa inu, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza, amene inu simunawamvere,+

  • Yeremiya 29:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndidzawachitira zimenezi chifukwa chakuti sanamvere mawu anga amene ndinali kuwatumizira kudzera mwa atumiki anga aneneri. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kutumiza atumiki angawo,’+ watero Yehova.

      “‘Inunso simunandimvere,’+ watero Yehova.

  • Yeremiya 35:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ndinali kukutumizirani atumiki anga onse aneneri,+ kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza. Ndinali kuwatuma uthenga wakuti, ‘Bwererani chonde, aliyense asiye njira zake zoipa+ ndipo sinthani zochita zanu kuti zikhale zabwino.+ Musatsatire milungu ina ndi kuitumikira.+ Mupitirize kukhala m’dziko limene ndinakupatsani, inuyo ndi makolo anu.’+ Koma inu simunatchere khutu kapena kundimvera.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena