10 Amuna a ku Perisiya,+ ku Ludi+ ndi ku Puti+ anali m’gulu lako lankhondo, anali m’gulu la asilikali ako. Amuna amenewa anali kupachika zishango ndi zisoti mwa iwe.+ Iwo ndi amene anakuchititsa kukhala waulemerero.
9 Mphamvu zake zonse zinali kuchokera ku Itiyopiya komanso ku Iguputo,+ ndipo zinali zopanda malire. Anthu a ku Puti komanso a ku Libiya anali kumuthandiza.+