Yeremiya 1:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pakuti Yehova wanena kuti,+ ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto. Ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi kukhazikitsa mpando wake wachifumu pazipata za Yerusalemu.+ Iwo adzaukira mpanda wake wonse ndi mizinda yonse ya Yuda.+ Yeremiya 47:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Yehova anati: “Taonani! Madzi akubwera+ kuchokera kumpoto+ ndipo madzi ake ndi achigumula. Adzamiza dziko ndi zonse zokhala mmenemo.+ Adzamizanso mzinda ndi zonse zokhala mmenemo. Amuna adzalira mokuwa, ndipo aliyense wokhala m’dzikolo adzalira mofuula.+ Ezekieli 30:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononga khamu la ku Iguputo pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadirezara, mfumu ya Babulo.+
15 Pakuti Yehova wanena kuti,+ ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto. Ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi kukhazikitsa mpando wake wachifumu pazipata za Yerusalemu.+ Iwo adzaukira mpanda wake wonse ndi mizinda yonse ya Yuda.+
2 Yehova anati: “Taonani! Madzi akubwera+ kuchokera kumpoto+ ndipo madzi ake ndi achigumula. Adzamiza dziko ndi zonse zokhala mmenemo.+ Adzamizanso mzinda ndi zonse zokhala mmenemo. Amuna adzalira mokuwa, ndipo aliyense wokhala m’dzikolo adzalira mofuula.+
10 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononga khamu la ku Iguputo pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadirezara, mfumu ya Babulo.+