5 Mtima wanga ukulirira Mowabu.+ Anthu ake athawira kutali, ku Zowari+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Aliyense akumakwera mtunda wa Luhiti+ akulira. Panjira yopita ku Horonaimu,+ iwo akufuula kwambiri chifukwa cha tsokalo.
34 “‘Kulira kochokera ku Hesiboni+ kudzamveka ku Eleyale+ ndi ku Yahazi.+ Kulira kochokera ku Zowari+ kudzamveka ku Horonaimu+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Madzi a ku Nimurimu+ nawonso adzawonongedwa.