5 Mtima wanga ukulirira Mowabu.+ Anthu ake athawira kutali, ku Zowari+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Aliyense akumakwera mtunda wa Luhiti+ akulira. Panjira yopita ku Horonaimu,+ iwo akufuula kwambiri chifukwa cha tsokalo.
11 N’chifukwa chake mkati mwanga mukunjenjemera ngati zingwe za zeze chifukwa cha Mowabu,+ ndipo m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha Kiri-hareseti.+