Yeremiya 4:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Wowonongayo akubwera ngati mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala.+ Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+ Wachoka m’malo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chodabwitsa. Mizinda yanu idzagwa ndi kukhala mabwinja moti sipadzapezeka wokhalamo.+ Zekariya 11:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Tamverani! Abusa akulira mofuula+ chifukwa ulemerero wawo watha.+ Tamverani! Mikango yamphamvu ikubangula mofuula chifukwa nkhalango zowirira, za m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano zawonongedwa.+
7 Wowonongayo akubwera ngati mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala.+ Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+ Wachoka m’malo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chodabwitsa. Mizinda yanu idzagwa ndi kukhala mabwinja moti sipadzapezeka wokhalamo.+
3 Tamverani! Abusa akulira mofuula+ chifukwa ulemerero wawo watha.+ Tamverani! Mikango yamphamvu ikubangula mofuula chifukwa nkhalango zowirira, za m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano zawonongedwa.+