11 Anthu ena onse amene anatsala mumzindamo, ndi anthu amene anapita kumbali ya mfumu ya Babulo, ndiponso anthu ena onse,+ Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawatenga kupita nawo ku ukapolo.+
18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse,+ zazikulu+ ndi zazing’ono, za m’nyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma+ cha m’nyumba ya Yehova, chuma cha mfumu+ ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse n’kupita nacho ku Babulo.