Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 29:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Ndiyeno zikachitika kuti wina amene wamva mawu a lumbiro+ ili, walankhula modzitama mumtima mwake kuti, ‘Ndidzakhala ndi mtendere+ ngakhale kuti ndidzayenda motsatira zofuna za mtima wanga,’+ koma ali ndi cholinga chowononga wina aliyense, mofanana ndi kukokolola mtengo wothiriridwa bwino ndi wosathiriridwa womwe,

  • Yeremiya 5:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Koma anthu awa ali ndi mtima wouma ndi wopanduka. Achoka panjira yanga ndipo akuyenda m’njira yawo.+

  • Yeremiya 23:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+

  • Ezekieli 3:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma a nyumba ya Isiraeli sakafuna kukumvera, chifukwa iwo safuna kundimvera.+ Pakuti anthu onse a nyumba ya Isiraeli ndi amakani ndi osamva.+

  • Hoseya 4:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Isiraeli wakhala wamakani* ngati ng’ombe yamakani.+ Choncho kodi Yehova angawawete ngati nkhosa yamphongo yaing’ono pamalo otakasuka?

  • Zekariya 7:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iwo anaumitsa mtima wawo+ ngati mwala wolimba kwambiri kuti asamvere malamulo+ ndi mawu a Yehova wa makamu, amene anawatumizira mwa mzimu wake+ kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa makamu anakwiya kwambiri.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena