Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 2:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ana a Isiraeli sanamvere ngakhale oweruza awo, koma anachita chiwerewere+ ndi milungu ina+ ndi kuigwadira. Iwo anapatuka mwamsanga panjira imene makolo awo anayendamo. Makolo awo anayenda m’njira imeneyo mwa kumvera malamulo a Yehova,+ koma iwo sanachite mofanana ndi makolo awo.

  • 1 Samueli 8:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Zinthu zonse zimene akhala akuchita kuyambira pa tsiku limene ndinawatulutsa mu Iguputo+ mpaka lero, kundisiya+ n’kumakatumikira milungu ina,+ n’zimenenso akuchitira iwe.

  • 2 Mafumu 22:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 chifukwa chakuti andisiya n’kumakafukiza nsembe yautsi kwa milungu ina+ kuti andikwiyitse ndi ntchito zonse za manja awo.+ Choncho mkwiyo wanga wayakira malo ano ndipo suzimitsidwa.’”’+

  • 2 Mbiri 28:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ahaziyo anayamba kupereka nsembe kwa milungu+ ya ku Damasiko+ imene inali kumuukira, ndipo anati: “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a Siriya ikuwathandiza,+ ndipereka nsembe kwa iyo kuti inenso indithandize.”+ Koma milunguyo inakhala chopunthwitsa kwa iye ndi kwa Aisiraeli onse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena