18 Koma ine lero ndakusandutsa mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, mzati wachitsulo ndi makoma amkuwa+ kuti dziko lonseli lisakugonjetse.+ Ndithu kuti mafumu a Yuda, akalonga ake, ansembe ake ndi anthu a m’dzikoli asakugonjetse.+
9 Ndachititsa chipumi chako kukhala ngati mwala wa dayamondi, cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi.+ Usawaope,+ ndipo usachite mantha ndi nkhope zawo,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.”+