-
Yeremiya 34:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 “Choncho Yehova wanena kuti, ‘Inu simunamvere mawu anga moti simunapitirize kulengeza ufulu,+ aliyense kwa m’bale wake ndi kwa mnzake. Tsopano ine ndikulengeza ufulu kwa inu,’+ watero Yehova. ‘Inu mudzafa ndi lupanga,+ mliri+ ndi njala yaikulu.+ Ndidzakusandutsani chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho.+
-
-
Ezekieli 5:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Gawo limodzi la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzafa ndi mliri+ ndipo adzatha ndi njala pakati pako.+ Gawo lina la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzaphedwa ndi lupanga mokuzungulira. Gawo lomaliza la magawo atatu a anthu a mtundu wako ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi,+ ndipo ndidzawatsatira nditasolola lupanga.+
-