Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wowononga,+ iye ndi Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.*+

  • Salimo 21:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Mudzawakhalitsa ngati oponyedwa mung’anjo yamoto pa nthawi ya kuonekera kwanu.+

      Yehova adzawameza mu mkwiyo wake, ndipo moto udzawanyeketsa.+

  • Yesaya 30:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Malo otchedwa Tofeti*+ owonongerako Asuri akonzedwa kale. Malowo akonzedweranso mfumu yawo.+ Malo amene iye wakonzawo ndi ozama ndipo kuli moto waukulu ndi nkhuni zambiri. Mpweya wa Yehova ukuyatsa malowo ngati mtsinje wa sulufule.+

  • Yeremiya 21:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Inu a m’nyumba ya Davide,+ Yehova wanena kuti: “M’mawa uliwonse+ muziweruza mwachilungamo,+ ndipo muzilanditsa munthu kwa anthu achinyengo amene akufuna kumulanda katundu.+ Muzitero kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto+ ndi kukutenthani popanda wouzimitsa chifukwa cha kuipa kwa zochita zanu.”’+

  • Ezekieli 22:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu amenewa ndili wokwiya ndiponso waukali. Ndidzawasonkhanitsa ngati mmene anthu amasonkhanitsira siliva, mkuwa, chitsulo,+ mtovu ndi tini m’ng’anjo kuti zinthu zimenezi azikolezere+ moto ndi kuzisungunula.+ Choncho anthu inu ndidzakukolezerani moto ndi kukusungunulani.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena