Levitiko 26:39 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 39 Otsala pakati panu, adzazunzika+ chifukwa cha zolakwa zawo m’mayiko a adani awo. Iwo adzazunzika chifukwa cha zolakwa za makolo awo,+ mmene makolowo anazunzikira. Ezara 9:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Kenako ndinayamba kunena kuti:+ “Inu Mulungu wanga, ndikuchita manyazi+ kuti ndikweze nkhope yanga kwa inuyo Mulungu wanga, chifukwa zolakwa zathu+ zachuluka pamutu pathu ndipo machimo athu achuluka kwambiri mpaka kufika kumwamba.+ Nehemiya 9:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 “Koma iwo anakhala osamvera+ ndipo anakupandukirani.+ Anapitiriza kufulatira chilamulo chanu,+ ndipo anapha aneneri anu+ amene anali kuwalimbikitsa kuti abwerere kwa inu.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani.+ Yeremiya 31:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 “Ndamva Efuraimu akudzilirira+ kuti, ‘Mwandidzudzula kuti ndiwongolere.+ Ndinali ngati mwana wa ng’ombe wosaphunzitsidwa.+ Ndithandizeni kubwerera ndipo ndidzabwereradi,+ pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.+
39 Otsala pakati panu, adzazunzika+ chifukwa cha zolakwa zawo m’mayiko a adani awo. Iwo adzazunzika chifukwa cha zolakwa za makolo awo,+ mmene makolowo anazunzikira.
6 Kenako ndinayamba kunena kuti:+ “Inu Mulungu wanga, ndikuchita manyazi+ kuti ndikweze nkhope yanga kwa inuyo Mulungu wanga, chifukwa zolakwa zathu+ zachuluka pamutu pathu ndipo machimo athu achuluka kwambiri mpaka kufika kumwamba.+
26 “Koma iwo anakhala osamvera+ ndipo anakupandukirani.+ Anapitiriza kufulatira chilamulo chanu,+ ndipo anapha aneneri anu+ amene anali kuwalimbikitsa kuti abwerere kwa inu.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani.+
18 “Ndamva Efuraimu akudzilirira+ kuti, ‘Mwandidzudzula kuti ndiwongolere.+ Ndinali ngati mwana wa ng’ombe wosaphunzitsidwa.+ Ndithandizeni kubwerera ndipo ndidzabwereradi,+ pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.+