19 Kwa iwo kudzamveka mawu oyamikira ndi phokoso la kuseka kwa anthu.+ Ndidzawachulukitsa moti sadzakhala ochepa.+ Ndidzachulukitsa chiwerengero chawo moti sadzakhala kagulu kakang’ono ka anthu.+
27 “Taonani! Masiku adzafika, pamene ndidzachititsa nyumba ya Isiraeli ndi nyumba ya Yuda kukhalanso ndi anthu ochuluka ndiponso ziweto zochuluka,” watero Yehova.+