2 M’masomphenya a Mulungu, iye ananditengera m’dziko la Isiraeli ndi kundikhazika paphiri lalitali kwambiri.+ Mbali ya kum’mwera paphiripo panali chinachake chooneka ngati mzinda.+
20 Anayeza malo onsewo mbali zonse zinayi. Malo onsewo anali ndi mpanda+ wokwana mabango 500 m’litali ndi mabango 500 m’lifupi mwake.+ Mpandawo unali kusiyanitsa zinthu zopatulika ndi zinthu zodetsedwa.+