28 Ntchito yawo inali yotumidwa ndi ana a Aroni+ pa utumiki wa panyumba ya Yehova m’mabwalo a nyumbayo,+ m’zipinda zodyeramo,+ pa ntchito yoyeretsa chinthu chilichonse chopatulika,+ ndiponso pa ntchito yotumikira panyumba ya Mulungu woona.
32 Ana a Leviwa analinso ndi ntchito yolondera+ chihema chokumanako, malo oyera,+ ndiponso yolondera abale awo, ana a Aroni, pa utumiki wa panyumba ya Yehova.+