31 Anali kutumikiranso nthawi iliyonse yopereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa masabata,+ pa masiku okhala mwezi,+ ndi pa nyengo za chikondwerero.+ Nthawi zonse anali kutumikira popereka nsembezo kwa Yehova, malinga ndi ziwerengero zake, komanso potsata lamulo lake.