Genesis 29:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Anakhalanso ndi pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Tsopano nditamanda Yehova.” Choncho Leya anatcha mwanayo, Yuda.*+ Atabereka mwana ameneyu, anayamba waleka kubereka. Yoswa 15:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Gawo+ la fuko la ana a Yuda potsata mabanja awo linkafika kumalire a Edomu,+ ndi kuchipululu cha Zini,+ mpaka kothera kwa Negebu,+ kum’mwera. Yoswa 19:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Cholowa cha ana a Simiyoni chinali m’gawo la ana a Yuda chifukwa ana a Yuda gawo lawo linawakulira.+ Choncho ana a Simiyoni anapatsidwa malo pakati pa cholowa chawo.+
35 Anakhalanso ndi pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Tsopano nditamanda Yehova.” Choncho Leya anatcha mwanayo, Yuda.*+ Atabereka mwana ameneyu, anayamba waleka kubereka.
15 Gawo+ la fuko la ana a Yuda potsata mabanja awo linkafika kumalire a Edomu,+ ndi kuchipululu cha Zini,+ mpaka kothera kwa Negebu,+ kum’mwera.
9 Cholowa cha ana a Simiyoni chinali m’gawo la ana a Yuda chifukwa ana a Yuda gawo lawo linawakulira.+ Choncho ana a Simiyoni anapatsidwa malo pakati pa cholowa chawo.+