4 Malo oyerawa adzakhale gawo la ansembe m’dzikoli.+ Ansembewo ndi atumiki a pamalo opatulika ndipo amayandikira kwa Yehova ndi kumutumikira.+ Malo amenewa adzakhale awo kuti adzamangepo nyumba zawo. Adzakhalenso malo opatulika omangapo nyumba yopatulika.