3 Ahazi anafukiza nsembe yautsi+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Iye anawotcha ana ake+ pamoto mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+
10 Chotero ine ndinalowa, ndipo ndinaona kuti pamakoma anajambulapo zithunzi+ za nyama iliyonse yokwawa, za chilombo chilichonse chonyansa+ ndi za mafano onse onyansa a nyumba ya Isiraeli.+ Pamakoma onse anajambulapo zithunzizo mochita kugoba.