Yesaya 6:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.+ Zekariya 7:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 ‘Chotero ndinawabalalitsira ku mitundu yonse ya anthu+ imene sanali kuidziwa,+ ngati kuti atengedwa ndi mphepo yamkuntho. Dzikoli analisiya labwinja, popanda munthu wodutsamo kapena kuyendayendamo.+ Iwo anasandutsa dziko losiririka+ kukhala chinthu chodabwitsa.’”
11 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.+
14 ‘Chotero ndinawabalalitsira ku mitundu yonse ya anthu+ imene sanali kuidziwa,+ ngati kuti atengedwa ndi mphepo yamkuntho. Dzikoli analisiya labwinja, popanda munthu wodutsamo kapena kuyendayendamo.+ Iwo anasandutsa dziko losiririka+ kukhala chinthu chodabwitsa.’”