Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 7:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Zitatero, Samueli anauza nyumba yonse ya Isiraeli kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova+ ndi mtima wanu wonse, chotsani milungu yachilendo pakati panu.+ Muchotsenso zifaniziro za Asitoreti,+ ndi kulunjikitsa mitima yanu kwa Yehova mosayang’ananso kwina,+ ndi kutumikira iye yekha. Mukatero, adzakupulumutsani m’manja mwa Afilisiti.”+

  • 1 Mafumu 8:47
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 ndiyeno iwo n’kuzindikira kulakwa kwawo m’dziko limene anawatengeralo+ n’kulapa,+ ndipo akapempha+ chifundo kwa inu m’dziko la adani awo amene awagwira,+ n’kunena kuti, ‘Tachimwa,+ tachita zolakwa,+ ndiponso tachita zinthu zoipa,’+

  • Yesaya 55:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+

  • Yeremiya 8:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 N’chifukwa chiyani anthu a mu Yerusalemu ali osakhulupirika ndipo akhalabe osakhulupirika kwa nthawi yaitali chonchi? Iwo akupitiriza kuchita zachinyengo+ ndipo akana kubwerera.+

  • Machitidwe 3:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Chotero lapani+ ndi kutembenuka+ kuti machimo anu afafanizidwe,+ ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa+ zibwere kuchokera kwa Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena