21 Iye anati: “Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida!+ chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu akanakhala atalapa kalekale, atavala ziguduli* ndi kukhala paphulusa.+
41 Anthu a ku Nineve adzaimirira pa chiweruzo limodzi ndi m’badwo uwu+ ndipo adzautsutsa,+ chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa Yona ali pano.