3 “‘Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zanu zonse.+ Limeneli ndi tsiku la msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito iliyonse chifukwa limeneli ndi sabata la Yehova kulikonse kumene mungakhale.+
24 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘M’mwezi wa 7,+ pa tsiku loyamba m’mweziwo, muzipuma pa ntchito zanu zonse. Limeneli ndi tsiku la chikumbutso, tsiku loliza lipenga,+ tsiku la msonkhano wopatulika.+
32 Ili ndi sabata lopuma pa ntchito zanu zonse,+ ndipo muzidzisautsa+ madzulo pa tsiku la 9 m’mweziwo. Muzisunga sabata kuyambira madzulo kufikira madzulo tsiku lotsatira.”
11 Chaka cha 50 ndi Chaka cha Ufulu kwa inu.+ Musalime minda yanu kapena kukolola mbewu zomera zokha, kapenanso kukolola mphesa za m’mitengo yosadulirayo.+