4 “‘Koma pakati pa nyama zimene zimabzikula ndi zimene zili ndi ziboda zogawanika, izi zokha musadye: Ngamila, chifukwa imabzikula koma ziboda zake n’zosagawanika. Nyama imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu.+
13 “‘Pakati pa zolengedwa zouluka,+ izi zikhale zonyansa kwa inu. Siziyenera kudyedwa chifukwa ndi zonyansa: Chiwombankhanga,+ nkhwazi ndi muimba wakuda.