-
Danieli 4:32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 ndipo akuthamangitsa pakati pa anthu. Uyamba kukhala pakati pa nyama zakutchire+ ndipo uzidzadya udzu ngati ng’ombe. Ndiyeno padutsa nthawi zokwanira 7 kufikira utadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa.’”+
-
-
Danieli 5:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo mtima wake unasinthidwa n’kukhala ngati wa nyama. Anayamba kukhala limodzi ndi abulu akutchire+ ndipo anali kudya udzu ngati ng’ombe. Thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba,+ kufikira pamene anadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti akafuna kuika munthu aliyense kuti akhale wolamulira, amamuika.+
-