Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mateyu 25:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 “Mwana wa munthu+ akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse,+ adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero.+

  • Yohane 3:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ndipo palibe munthu amene anakwera kumwamba+ koma Mwana wa munthu+ yekha, amene anatsika kuchokera kumwambako.+

  • Machitidwe 7:56
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 56 Ndipo ananena kuti: “Taonani! Ndikuona kumwamba kotseguka,+ ndipo Mwana wa munthu+ waimirira kudzanja lamanja la Mulungu.”+

  • Afilipi 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Sanatero ayi, koma anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo,+ ndi kukhala wofanana ndi anthu.+

  • Aheberi 2:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Chotero, popeza kuti “ana” amenewo onse ndi amagazi ndi mnofu, iyenso anakhala wamagazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake,+ awononge+ Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+

  • Chivumbulutso 1:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pakati pa zoikapo nyalezo, panali wina wooneka ngati mwana wa munthu+ atavala chovala chofika kumapazi, atamanga lamba wagolide pachifuwa.

  • Chivumbulutso 14:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Nditayang’ana, ndinaona mtambo woyera. Pamtambopo panakhala winawake ngati mwana wa munthu,+ atavala chisoti chachifumu chagolide+ kumutu kwake, chikwakwa chakuthwa chili m’dzanja lake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena