Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 8:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Kenako ndinalamula kuti tisale kudya tili kumtsinje wa Ahava kuja, kuti tidzichepetse+ pamaso pa Mulungu wathu ndi kumupempha kuti atisonyeze njira yoyenera+ kwa ife, ana athu,+ ndi katundu wathu yense.

  • Esitere 4:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndipo m’zigawo zonse,+ kulikonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, Ayuda anali ndi chisoni kwambiri+ ndipo anali kusala kudya,+ kubuma ndi kulira mofuula. Ambiri anayala ziguduli+ ndi kuwazapo phulusa+ kuti agonepo.

  • Salimo 35:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iwo akadwala ndinali kuvala chiguduli,+

      Ndinali kusautsa moyo wanga mwa kusala kudya.+

      Ndipo mapemphero anga anali kubwerera kwa ine osayankhidwa.+

  • Salimo 69:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndipo ndinalira ndi kusala kudya chifukwa cha moyo wanga,+

      Koma anthu anali kungonditonza chifukwa cha zimenezo.+

  • Ezekieli 27:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Adzadzimeta mpala chifukwa cha iwe+ ndi kuvala ziguduli+ ndipo adzakulirira mowawidwa mtima.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena