Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 30:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Inu mudzatumikira Yehova Mulungu wanu ndi Davide mfumu yanu+ imene ndidzakuutsirani.”+

  • Ezekieli 34:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndidzazipatsa m’busa mmodzi,+ amene ndi mtumiki wanga Davide,+ ndipo adzazidyetsa. Iye adzakhala m’busa wawo ndipo adzazidyetsadi.+

  • Ezekieli 37:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ndidzawaphatikiza kuti akhale mtundu umodzi m’dzikolo,+ m’mapiri a Isiraeli. Onsewo adzakhala ndi mfumu imodzi+ ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawanika kukhala maufumu awiri.+

  • Amosi 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “‘Pa tsiku limenelo, ndidzautsa+ nyumba+ ya Davide imene inagwa,+ ndi kukonza mmene khoma* lake linawonongeka. Ndidzautsa mabwinja ake ndipo ndidzaimanga kuti ikhale ngati masiku akale.+

  • Luka 1:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.+ Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu+ wa Davide atate wake.+

  • Chivumbulutso 22:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu+ ndi mbadwa+ ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena