46 “‘Mkulu wako amene akukhala kumanzere kwako ndiye Samariya+ ndi midzi yake yozungulira.+ Mng’ono wako, amene akukhala mbali ya kudzanja lako lamanja ndi Sodomu+ ndi midzi yake yozungulira.+
5 “Izi zichitika chifukwa cha kupanduka kwa Yakobo ndiponso chifukwa cha machimo a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi wachititsa kupanduka kwa Yakobo ndani? Kodi si anthu a ku Samariya?+ Wachititsa ndani kuti Yuda akhale ndi malo okwezeka?+ Si anthu a ku Yerusalemu kodi?