1 Mafumu 17:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Koma patapita masiku angapo, mtsinjewo unauma,+ chifukwa padziko lapansi sipanabwere mvula. 1 Mafumu 18:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ndiyeno Ahabu anauza Obadiya kuti: “Pita m’dzikoli, ukayendere akasupe onse a madzi ndi zigwa* zonse. Mwina tikhoza kupeza udzu wobiriwira+ woti tidyetse mahatchi ndi nyulu, kuti nyamazi zisapitirize kufa.”+ Yeremiya 14:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya pa nkhani ya chilala+ ndi awa:
5 Ndiyeno Ahabu anauza Obadiya kuti: “Pita m’dzikoli, ukayendere akasupe onse a madzi ndi zigwa* zonse. Mwina tikhoza kupeza udzu wobiriwira+ woti tidyetse mahatchi ndi nyulu, kuti nyamazi zisapitirize kufa.”+